
Written by Paul J Bucknell on January, 24, 2024
Gawo 1: Masomphenya a Umodzi wa Mpingo
Masomphenya ndi Ndondomeko za mpingo zimayenera kukhazikika pa Mau a Mulungu. Pamene talandira nzeru ndi kutsatira Malangizo ake, maganizidwe athu osinthika akhoza Kugwira ntchito molunjika kukukwaniritsidwa kwa umodzi wa mpingo mosasemphana ndi Malangizo opezeka m’Mau a Mulungu. Ndichinthu chofunikira kwambiri kuwona chinthu cha mtengo wapatali umodzi wa mkazi wa Khristu ndi kugwirira ntchito pamodzi pa zinthu zimene zimatimangirira pamodzi – Yesu Khristu – kusiyana ndi zimene zimatigawanitsa.